Zokhudza Mau a Mulungu

MauaBaibulo imabweletsa Mau a Mulungu kwa anthu pa intaneti. Timachita izi kudzera pa tsamba la Facebook komanso webusaiti ino. Timapeleka malingaliro tsiku ndi tsiku kuchokera m’Baibulo kuti zilimbikitse, ziphunzitse, komanso kutsutsa. Pa Facebook kawirikawiri izi zimakhala zonenedwa zifupizifupi za Baibulo komanso machezedwe a Baibulo. Pa webusaiti iyi timayikapo zolembedwa zitalizitali komanso mavidiyo zokutsogolerani kuzamitsidwa m’Mawu a Mulungu. Ngati muli ndi mafunso okhudzana ndi Baibulo kapena chikhulupiliro cha chikhristu, chonde tilembeleni. Timayesetsa kuyankha nthawi zonse. MauaBaibulo ndi utumiki wa GlobalRize. MauaBaibulo linayambitsidwa ndipo likutsogoleledwa ndi Marten Visser. Marten ndi m’busa wa ku Netherlands yemwe ali ndi zaka zambiri zotumikira ngati wakufalitsa uthenga pakati pa anthu othawa nkhondo komanso ngati okhazikitsa mipingo ku Thailand. Gulu lomwe limathandizila pa MauaBaibulo limachokera m’maiko osiyanasiyana, kuphatikizapo Malaysia, Philippines, Thailand, UK, komanso USA. Kuonjezera pa tsamba la Chichewa, MauaBaibulo limapezekanso mu zinenero zina khumi ndi zinayi pa Facebook.

Share post